Ezekiel 38:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikukaŵalanda chuma chao ndi kufunkha zinthu zao. Ndikukathira nkhondo anthu okhala m'mizinda imene kale inali mabwinja. Ndidzalimbananso ndi anthu amene adasonkhana kuchokera ku maiko ambiri. Anthuwo ali ndi zoŵeta ndi katundu wochuluka, ndiponso amakhala pakatikati pa dziko lapansi.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kulanda ndi kufunkha zao, kubweza dzanja lako liononge mopasuka muli anthu tsopano, liononge mtundu wa anthu osonkhanidwa mwa amitundu, odzionera zoweta ndi chuma, okhala pakati pa dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipita kukalanda chuma chawo ndi kukafunkha zinthu zawo. Ndidzalimbana ndi midzi imene kale inali mabwinja. Ndikathira nkhondo anthu amene anasonkhanitsidwa kuchokera kwa anthu a mitundu ina. Iwowa ali ndi ziweto zambiri, katundu wochuluka ndiponso amakhala pakatikati pa dziko lapansi.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kulanda ndi kufunkha zao, kubweza dzanja lako liononge mopasuka muli anthu tsopano, liononge mtundu wa anthu osonkhanidwa mwa amitundu, odzionera zoweta ndi cuma, okhala pakati pa dziko.