Ezekiel 38:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a ku Sheba ndi ku Dedani, ndiponso amalonda a ku Tarisisi ndi midzi yake yonse, adzafunsa kuti, ‘Kodi kutereku, ukudzafunkha? Kodi wasonkhanitsa gulu lako lankhondo kudzanyamula zofunkha, kudzatenga siliva ndi golide, kudzalanda ziŵeto ndi katundu, kuti zikhale zofunkha zochuluka?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sheba, ndi Dedani, ndi amalonda a Tarisisi, ndi misona yake yonse ya mikango adzati kwa iwe, Wadza kodi kudzafunkha? Wasonkhanitsa kodi msonkhano wako kulanda, kuchoka nazo siliva ndi golide, kuchoka nazo zoweta ndi chuma, kulanda zankhondo zambiri?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Seba, a ku Dedani ndiponso amalonda a ku Tarisisi pamodzi ndi midzi yake yonse adzakufunsa kuti, ‘Kodi wabwera kudzafunkha? Kodi wasonkhanitsa gulu lako la nkhondo kudzalanda chuma, kudzatenga siliva ndi golide, ziweto ndi katundu kuti zikhale zofunkha zochuluka?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Seba, ndi Dedani, ndi amalonda a Tarisi, ndi misona yace yonse ya mikango adzati kwa iwe, Wadza kodi kudzafunkha? wasonkhanitsa kodi msonkhano wako kulanda, kucoka nazo siliva ndi golidi, kucoka nazo zoweta ndi cuma, kulanda zankhondo zambiri?