Ezekiel 38:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake, iwe mwana wa munthu, ulalike ndipo uuze Gogi kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pa nthaŵi imene anthu anga Aisraele adzakhale mwamtendere, udzanyamuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake nenera, wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa Gogi, Atero Ambuye Yehova, Tsiku ilo, pokhala mosatekeseka anthu anga Israele, sudzachidziwa kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake, iwe mwana wa munthu, nenera ndipo uwuze Gogi kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene anthu anga adzakhala pa mtendere, iwe udzanyamuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace nenera, wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa Gogi, Atero Ambuye Yehova, Tsiku ilo, pokhala mosatekeseka anthu anga Israyeli, sudzacidziwa kodi?