Ezekiel 38:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzachokera kwanu ku mbali zakutali kumpoto, pamodzi ndi mitundu yambiri ya anthu, onsewo okwera pa akavalo, gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo udzatuluka m'malo mwako m'malekezero a kumpoto, iwe ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe, onsewo apakavalo, msonkhano waukulu ndi nkhondo yaikulu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzabwera kuchokera ku dziko lako kutali kumpoto, iwe pamodzi ndi mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe, onse okwera akavalo, gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo udzaturuka m'malo mwako m'malekezero a kumpoto, iwe ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe, onsewo apakavalo, msonkhano waukuru ndi nkhondo yaikuru;