Ezekiel 38:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzabwera kudzalimbana ndi anthu anga Aisraele, ngati namondwe woononga dziko lapansi. Masiku amenewo iwe Gogi ndidzakuyambanitsa ndi dziko langa kuti anthu a mitundu yonse adzandidziŵe, pamene ndidzaonetse kuyera kwanga pa zimene ndidzakuchite iweyo Gogi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo udzakwerera anthu anga Israele ngati mtambo wakuphimba dziko; kudzachitika masiku otsiriza ndidzabwera nawe ulimbane nalo dziko langa, kuti amitundu andidziwe, pozindikiridwa Ine woyera mwa iwe, Gogi, pamaso pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzabwera kudzalimbana ndi anthu anga Aisraeli ngati mtambo wophimba dziko. Masiku amenewo, iwe Gogi, ndidzabwera nawe kuti ulimbane ndi dziko langa, kuti anthu a mitundu ina andidziwe Ine, pamene ndidzaonetsa kuyera kwanga pa zimene ndidzakuchite iweyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo udzakwerera anthu anga Israyeli ngati mtambo wakuphimba dziko; kudzacitika masiku otsiriza ndidzabwera nawe ulimbane nalo dziko langa, kuti amitundu andidziwe, pozindikiridwa Ine woyera mwa iwe, Gogi, pamaso pao.