Ezekiel 38:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Kodi iwe si ndiwe amene ndidalankhula za iwe masiku amakedzana, kudzera mwa atumiki anga aneneri a ku Israele? Pa zaka zambiri iwo ankalengeza kuti ndidzautsa iwe kuti udzalimbane ndi Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Ambuye Yehova, Kodi iwe ndiwe iye amene ndinanena za iye masiku akale mwa atumiki anga aneneri a Israele, akunenera masiku aja za zaka za m'tsogolo, kuti ndidzabwera nawe kulimbana nao?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi iwe si amene ndinayankhula za iwe masiku amakedzana kudzera mwa atumiki anga aneneri a Israeli? Pa zaka zambiri iwo ankalengeza kuti ndidzawutsa iwe kuti udzalimbane ndi Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Ambuye Yehova, Kodi iwe ndiwe iye amene ndinanena za iye masiku akale mwa atumiki anga aneneri a Israyeli, akunenera masiku aja za zaka za m'tsogolo, kuti ndidzabwera nawe kulimbana nao?