Ezekiel 38:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakuzunguza, ndidzakukola ndi mbedza m'kamwa mwako. Ndidzakutulutsira poyera, iweyo pamodzi ndi gulu lako lonse lankhondo, akavalo ndi okwerapo ake. Onsewo adzakhala atanyamula zishango ndi malihawo, malupanga ao ali osololasolola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzakutembenuza ndi kukowa m'chibwano mwako ndi zokowera, ndi kukutulutsa ndi nkhondo yako yonse, akavalo ndi apakavalo ovala mokwanira onsewo, msonkhano waukulu ndi zikopa zotchinjiriza, onsewo ogwira bwino malupanga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakuzunguza, ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako. Ndidzakutulutsa iweyo pamodzi ndi gulu lako lonse la nkhondo, akavalo ako ndi okwerapo ake. Onse adzakhala atanyamula zida za nkhondo, zishango ndi malihawo ndipo malupanga awo adzakhala osolola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzakutembenuza ndi kukowa m'cibwano mwako ndi zokowera, ndi kukuturutsa ndi nkhondo yako yonse, akavalo ndi apakavalo obvala mokwanira onsewo, msonkhano waukuru ndi zikopa zocinjiriza, onsewo ogwira, bwino malupanga;