Ezekiel 38:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakuitana patapita masiku ambiri. Zaka zikubwerazi, ndidzakuloŵetsa m'dziko lopulumuka ku nkhondo. Udzaŵapeza anthu atasonkhana kuchokera ku mitundu yambiri ya anthu, atakhazikika ku mapiri a Aisraele amene adaasiyidwa nthaŵi yaitali. Aisraelewo adaŵatulutsa pakati pa mitundu ya anthu, ndipo onsewo ali pa mtendere tsopano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atapita masiku ambiri udzakumbukirika; zaka zotsiriza udzalowa m'dziko lobwezedwa lopulumuka lupanga, losonkhanidwa lituluke m'mitundu yambiri ya anthu, pa mapiri a Israele, amene adakhala achipululu chikhalire; koma litulutsidwa m'mitundu ya anthu, ndipo adzakhala mosatekeseka onsewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakapita masiku ambiri ndidzakuyitana. Zaka zikubwerazi ndidzakulowetsa mʼdziko limene lapulumuka ku nkhondo. Anthu ake anasonkhanitsidwa kuchokera ku mitundu ya anthu ambiri nʼkukakhazikika pa mapiri a Israeli amene kwa nthawi yayitali anali ngati chipululu. Anthu onsewa tsopano akukhala mwa mtendere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atapita masiku ambiri udzakumbukirika; zaka zotsiriza udzalowa m'dziko lobwezedwa lopulumuka lupanga, losonkhanidwa lituruke m'mitundu yambiri ya anthu, pa mapiri a Israyeli, amene adakhala acipululu cikhalire; koma liturutsidwa m'mitundu ya anthu, ndipo adzakhala mosatekeseka onsewo.