Ezekiel 39:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Miyezi isanu ndi iŵiri itapita, adzasankha anthu odzayendera m'dziko lonselo, kuti azifunafuna mitembo imene idatsalira ndi kumaikwirira, motero adzaliyeretseratu dzikolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzasankha anthu akupitapitabe m'dziko, ndi pamodzi ndi opitapitawo anthu akuika mafupa otsala pamtunda, kuliyeretsa; pakutha miyezi isanu ndi iwiri adzapwaira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Patapita miyezi isanu ndi iwiri adzalemba ntchito anthu ena odzayenda mʼdziko lonse kufunafuna mitembo imene inatsalira nʼkumayikwirira. Choncho adzayeretseratu dzikolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzasankha anthu akupita-pitabe m'dziko, ndi pamodzi ndi opitapitawo anthu akuika mafupa otsala pamtunda, kuliyeretsa; pakutha miyezi isanu ndi iwiri adzapwaira.