Ezekiel 39:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndiye iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Chauta mau anga ndi aŵa: Uitane mbalame ndi nyama zonse zakuthengo, uziwuze kuti, ‘Sonkhanani mubwere kuno. Musonkhane kuchokera kumbali zonse. Mubwere ku phwando limene ndikukukonzerani ku mapiri a Israele. Phwando lake ndi lansembe. Kumeneko mudzadya nyama ndi kumwa magazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova, Nena kwa mbalame za mitundu yonse, ndi kwa nyama zonse za kuthengo, Memezanani, idzani, sonkhanani kumbali zonse, kudza kunsembe yanga imene ndikupherani, ndiyo nsembe yaikulu pa mapiri a Israele, kuti mudzadye nyama ndi kumwa mwazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Itana mbalame za mitundu yonse ndi zirombo zonse zakuthengo ndipo uziwuze kuti, ‘Sonkhanani ndipo bwerani kuchokera ku mbali zonse ku nsembe imene ndikukonzerani inu, nsembe yayikulu pa mapiri a Israeli. Kumeneko inu mudzadya mnofu ndi kumwa magazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova, Nena kwa mbalame za mitundu yonse, ndi kwa nyama zonse za kuthengo, Memezanani, idzani, sonkhanani ku mbali zonse, kudza ku nsembe yanga imene ndikupherani, ndiyo nsembe yaikuru pa mapiri a Israyeli, kuti mudzadye nyama ndi kumwa mwazi.