Ezekiel 39:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a m'maiko onse adzadziŵa kuti Aisraele adaatengedwa ukapolo chifukwa cha machimo ao, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho ndidaŵafulatira, ndipo ndidaŵapereka m'manja mwa adani ao. Motero onsewo adafa pa nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amitundu adzadziwa kuti nyumba ya Israele idalowa undende chifukwa cha mphulupulu zao, popeza anandilakwira Ine; ndipo ndinawabisira nkhope yanga; m'mwemo ndinawapereka m'dzanja la adani ao, nagwa iwo onse ndi lupanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti anthu a Israeli anatengedwa ukapolo chifukwa cha tchimo lawo, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho Ine ndinawabisira nkhope yanga ndi kuwapereka kwa adani awo. Motero anaphedwa pa nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amitundu adzadziwa kuti nyumba ya Israyeli idalowa undende cifukwa ca mphulupulu zao, popeza anandilakwira Ine; ndipo ndinawabisira nkhope yanga; m'mwemo ndinawapereka m'dzanja la adani ao, nagwa iwo onse ndi lupanga.