Ezekiel 39:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵabwezera kwao kuŵachotsa pakati pa mitundu ina ya anthu, ndi kuŵasonkhanitsa kuchokera ku maiko a adani aowo. Motero ndidzaonetsa pamaso pa mitundu yambiri ya anthu kuti ndinedi Woyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nditabwera nao kuchoka kwa mitundu ya anthu, nditawasokolotsa m'maiko a adani ao, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa iwo pamaso pa amitundu ambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawabwezeranso kwawo kuchokera pakati pa anthu a mitundu ina ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko a adani awo. Poteropo ndidzaonetsa pamaso pa anthu a mitundu yambiri kuti ndine Woyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nditabwera nao kucoka kwa mitundu ya anthu, nditawasokolotsa m'maiko a adani ao, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa iwo pamaso pa amitundu ambiri.