Ezekiel 39:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta Mulungu wao. Paja ndidaaŵatumiza ku ukapolo pakati pa mitundu ina ya anthu, kenaka ndidaŵabwezanso onse ku dziko lao, osasiyako ndi mmodzi yemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, popeza ndinalola atengedwe ndende kunka kwa amitundu, koma ndinawasonkhanitsanso akhale m'dziko lao, osasiyakonso mmodzi yense wa iwowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo, ngakhale kuti ndinawapereka ku ukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ine ndidzawasonkhanitsanso ku dziko lawo osasiyako wina mʼmbuyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, popeza ndinalola atengedwe ndende kumka kwa amitundu, koma ndinawasonkhanitsanso akhale m'dziko lao, osasiyakonso mmodzi yense wa iwowa.