Ezekiel 39:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzagwa ku mapiri a ku Israeleko, iweyo pamodzi ndi magulu ako onse ankhondo ndi onse amene amakuthandiza. Ndidzakusandutsa chakudya cha miimba ndi cha zilombo zakuthengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udzagwa pa mapiri a Israele, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zilombo za kuthengo, akuyese chakudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzagwa ku mapiri a ku Israeli, iwe ndi magulu ako onse ankhondo ndiponso mitundu ya anthu imene ili nawe. Ndidzakusandutsa chakudya cha mitundu yonse ya mbalame zodya nyama, ndiponso cha zirombo zakuthengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udzagwa pa mapiri a Israyeli, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zirombo za kuthengo, akuyese cakudya.