Ezekiel 39:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzamveketsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Aisraele. Ndipo sindidzalola kuti dzina langa liipitsidwenso. Anthu a m'maiko onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndine Woyera uja wa ku Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzadziwikitsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Israele, osalola dzina langa loyera aliipsenso; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Woyerayo wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Israeli. Sindidzalola kuti dzina langa liyipitsidwenso, ndipo mitundu ya anthu idzadziwa kuti Ine Yehova ndine Woyera mu Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzadziwikitsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Israyeli, osalola dzina langa loyera aliipsenso; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Woyerayo wa Israyeli.