Ezekiel 39:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Okhala m'mizinda ya Aisraele adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo zosiyidwa kuti azitenthe ngati nkhuni: ndiye kuti zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga ndi mikondo. Adzazisonkhere moto pa zaka zisanu ndi ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo okhala m'midzi ya Israele adzatuluka, nadzasonkha moto, nadzatentha zida za nkhondo, ndi zikopa zotchinjiriza, mauta, ndi mivi, ndi ndodo, ndi mikondo; ndipo adzasonkha moto nazo zaka zisanu ndi ziwiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pamenepo okhala mʼmizinda ya Israeli adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo kuti zikhale nkhuni ndipo adzazitentha; zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga za nkhondo ndi mikondo. Adzazisonkhera moto kwa zaka zisanu ndi ziwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo okhala m'midzi ya Israyeli adzaturuka, nadzasonkha moto, nadzatentha zida za nkhondo, ndi zikopa zocinjiriza, mauta, ndi mibvi, ndi ndodo, ndi mikondo; ndipo adzasonkha moto nazo zaka zisanu ndi ziwiri;