Ezekiel 4:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzadya buledi wako wophika ngati makeke abarele. Ndoŵe youma ya anthu ndiyo idzakhale nkhuni zako zophikira, ndipo uzidzaphikira kumene anthu angathe kukuwona.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo uzichidya ngati timikate ta barele, ndi kutiocha pamaso pao ndi zonyansa za munthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uzidya chakudya chako ngati momwe amadyera keke ya barele. Uzidzaphika chakudyacho anthu akuona pogwiritsa ntchito ndowe ya munthu ngati nkhuni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo uzicidya ngati timikate ta barele, ndi kutioca pamaso pao ndi zonyansa za munthu.