Ezekiel 4:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ine ndidati “Inu Ambuye Chauta, inetu sindidadziipitsepo motero pa chipembedzo. Kuyambira ubwana wanga mpaka lero lino, sindidadyepo nyama yofa yokha kapena yojiwa ndi zilombo, ndipo sindidadyepo nyama yonyansa pa zachipembedzo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwa, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ine ndinati, “Zisatero, Ambuye Yehova! Ine sindinadziyipitsepo pa zachipembedzo. Kuyambira ubwana wanga mpaka tsopano, sindinadyepo kanthu kalikonse kopezeka katafa kapena kophedwa ndi zirombo za kutchire. Palibe nyama yodetsedwa pa zachipembedzo imene inalowa pakamwa panga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! taonani, moyo wanga sunadetsedwa, pakuti ciyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye cinthu cakufa cokha, kapena cogwidwa ndi cirombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.