Ezekiel 4:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Iye adati, “Chabwino, ndidzakulola kuphikira ndoŵe ya ng'ombe m'malo mwa ndoŵe ya anthu, pophika buledi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa ine, Taona ndakuninkha ndowe ya ng'ombe m'malo mwa zonyansa za munthu, uotche mkate wako pamenepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Chabwino, ndidzakulola kuti uphike buledi wako ndi ndowe za ngʼombe mʼmalo mwa ndowe za munthu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Taona ndakuninkha ndowe ya ng'ombe m'malo mwa zonyansa za munthu, uoce mkate wako pamenepo.