Ezekiel 4:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Yerusalemu ndidzaŵachepetsera buledi wa tsiku ndi tsiku. Anthuwo buledi wao azidzachita woyesa, ndipo azidzadya mwankhaŵa. Madzi aonso azidzachita oyesa, nkumamwa mwamantha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndidzathyola mchirikizo, ndiwo chakudya, m'Yerusalemu; ndipo adzadya chakudyacho monga mwa muyeso, ndi mosamalira, nadzamwa madzi monga mwa muyeso, ndi kudabwa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Yerusalemu ndidzawachepetsera chakudya. Anthuwo adzadya chakudya chochita kuyeza ndipo azidzadya mwa nkhawa. Azidzamwanso madzi ochita kuyeza ndiponso mwa mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndidzatyola mcirikizo, ndiwo cakudya, m'Yerusalemu; ndipo adzadya cakudyaco monga mwa muyeso, ndi mosamalira, nadzamwa madzi monga mwa muyeso, ndi kudabwa;