Ezekiel 4:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Utenge chitsulo, uchiimike ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo. Uyang'anitsitse mzindawo, ndipo uumangire zithando zankhondo ndi kuuzinga kotheratu. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa Aisraele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nudzitengere chiwaya chachitsulo, ndi kuchiika ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mudziwo; nuulozetsere nkhope yako kuti umangidwire misasa, ndipo udzamangira misasa. Ichi chikhale chizindikiro cha nyumba ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka utenge chiwaya chachitsulo uchiyike ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo. Uyangʼanitsitse mzindawo ndipo udzakhala wozingidwa ndi nsanja za nkhondo. Choncho umangire nsanja zankhondo. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nudzitengere ciwaya cacitsulo, ndi kuciika ngati khoma lacitsulo pakati pa iwe ndi mudziwo; nuulozetsere nkhope yako kuti umangidwire misasa, ndipo udzamangira misasa. Ici cikhale cizindikilo ca nyumba ya Israyeli.