Ezekiel 4:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Utatha zimenezi, udzatembenuke nkugonera ku dzanja lamanja. Tsono udzasenze machimo a anthu a ku Yuda pa masiku makumi anai, tsiku lililonse kulinganiza ndi chaka chathunthu cha chilango chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo utatsiriza awa, ugonerenso mbali yako ya kumanja, ndi kusenza mphulupulu ya nyumba ya Yuda; ndakuikira masiku makumi anai, kuliyesa tsiku limodzi ngati chaka chimodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Utatha zimenezo udzagonerenso mbali ya kudzanja lamanja, ndipo udzasenza machimo a anthu a ku Yuda masiku makumi anayi, tsiku lililonse kuyimira chaka chimodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo utatsiriza awa, ugonerenso mbali yako ya kumanja, ndi kusenza mphulupulu ya nyumba ya Yuda; ndakuikira masiku makumi anai, kuliyesa tsiku limodzi ngati caka cimodzi.