Ezekiel 4:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsopano tenga tirigu ndi barele, nyemba ndi mphodza, mapira ndi mcheŵere, zonsezo uziike m'mbale imodzi, kenaka upange buledi. Uzidzadya pa masiku 390 amene udzakhale ukugonera mbali imodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udzitengerenso tirigu, ndi barele, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi mapira, ndi mawere, nuziike m'mbale imodzi, ndi kudzipangira mkate nazo; uzidyako monga mwa kuwerenga kwa masiku udzagonawo pambali pako, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono tenga tirigu ndi barele, nyemba ndi mphodza, mapira ndi mchewere; ndipo uyike zonsezi mʼmbale imodzi ndipo upange buledi wako. Uzidya pa masiku 390 amene udzakhala ukugonera mbali imodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udzitengerenso tirigu, ndi barele, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi mapira, ndi mawere, nuziike m'mbale imodzi, ndi kudzipangira mkate nazo; uzidyako monga mwa kuwerenga kwa masiku udzagonawo pambali pako, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai.