Ezekiel 40:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku mayambiriro a chaka, tsiku lakhumi la mwezi, chaka cha 25 cha ukapolo wathu, ndiye kuti patapita zaka khumi ndi zinai Yerusalemu ataonongedwa, dzanja la Chauta lidandigwira nkupita nane ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka cha makumi awiri ndi zisanu cha undende wathu, poyamba chaka, tsiku lakhumi lamwezi, chaka chakhumi ndi zinai atakantha mudziwo, tsiku lomwelo, dzanja la Yehova linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumayambiriro a chaka cha 25, cha ukapolo wathu, tsiku la khumi lamwezi, patapita zaka khumi ndi zinayi mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa, pa tsiku lomwelo dzanja la Yehova linali pa ine ndipo Iye anapita nane ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka ca makumi awiri ndi zisanu ca undende wathu, poyamba caka, tsiku lakhumi lamwezi, caka cakhumi ndi zinai atakantha mudziwo, tsiku lomwelo, dzanja la Mulungu linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko.