Ezekiel 40:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'kati mwa chipata chakuvumacho munali zipinda za alonda zitatu mbali iliyonse. Zitatu zonsezo zinali zolingana, ndipo mphuthu zake pa mbali zonse zinali zolingananso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi zipinda za alonda za kuchipata cha kum'mawa ndizo zitatu chakuno, ndi zitatu chauko, zitatuzi nza muyeso umodzimodzi, ndi mphuthuzo nza muyeso umodzimodzi, chakuno ndi chauko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼkati mwa chipata chakummawa munali zipinda za alonda zitatu mbali iliyonse. Zitatu zonsezo zinali zofanana, ndipo khonde la pakati pa zipindazo linali lofanana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi zipinda za alonda za ku cipata ca kum'mawa ndizo zitatu cakuno, ndi zitatu cauko, zitatuzi nza muyeso umodzimodzi, ndi mphuthuzo nza muyeso umodzimodzi, cakuno ndi cauko.