Ezekiel 40:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumaso kwa zipinda za alonda zija kunali kachipupa ka mita limodzi m'litali mwake ndi muufupi momwe. Zipinda zitatuzo zinali za mamita atatu mbali zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi pakhomo pa zipinda za alonda panali kakhoma ka mkono umodzi chakuno, ndi kakhoma ka mkono umodzi chauko; ndi zipinda za alonda mikono isanu ndi umodzi chakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi chauko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kutsogolo kwa chipinda chilichonse cha alonda kunali khoma lalifupi lotalika theka la mita, ndipo mbali iliyonse ya zipinda za alondazo inali yotalika mamita atatu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi pakhomo pa zipinda za alonda panali kakhoma ka mkono umodzi cakuno, ndi kakhoma ka mkono umodzi cauko; ndi zipinda za alonda mikono isanu ndi umodzi cakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi cauko.