Ezekiel 40:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adayesa kutalika kuchokera ku khoma lakumbuyo la chipinda chimodzi mpaka ku khoma la chipinda china, kuchokera ku chitseko mpaka kuchitseko china. Kutalika kwake kunali mamita 12 ndi theka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayesa chipata kuyambira kutsindwi la chipinda cha alonda chimodzi, kufikira kutsindwi la chinzake, kupingasa kwake ndiko mikono makumi awiri ndi isanu; makomo napenyana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anayeza kutalika kwa mulifupi mwa chipata cholowera, kuchokera ku khoma lakumbuyo la chipinda chimodzi mpaka ku khoma la chipinda china; kuchokera ku chitseko mpaka ku chitseko china. Kutalika kwake kunali mamita khumi ndi awiri ndi theka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayesa cipata kuyambira ku tsindwi la cipinda ca alonda cimodzi, kufikira ku tsindwi la cinzace, kupingasa kwace ndiko mikono makumi awiri ndi isanu; makomo napenyana.