Ezekiel 40:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makoma a zipinda zija ndiponso makoma a pakati pa zipindazo anali ndi mazenera. Khonde lam'kati linali nawonso mazenera m'kati mwake. Pa makoma onse adaazokotapo zithunzi za kanjedza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali mazenera amkati okhazikika pazipinda ndi m'makhoma a pakati pao, m'kati mwa chipata pozungulira ponse; momwemonso pazidundumwa; ndipo panali mazenera pozungulira ponse m'katimo, ndi pa nsanamirazo panali akanjedza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Makoma a zipinda ndiponso makoma a pakati pa zipindazo anali ndi mazenera. Khonde lamʼkati linalinso ndi mazenera mʼkati mwake. Pa makoma onsewo anajambulapo zithunzi za kanjedza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali mazenera a made okhazikika pazipinda ndi m'makhoma a pakati pao, m'kati mwa cipata pozungulira ponse; momwemonso pazidundumwa; ndipo panali mazenera pozungulira ponse m'katimo, pa nsanamirazo panali akanjedza.