Ezekiel 40:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono munthu uja adandiloŵetsa m'bwalo lakunja, ndipo ndidaona zipinda ndi mseu wamiyala kuzungulira bwalo lonse. Zipinda zonse pamodzi zinali makumi atatu ndipo zinkayang'ana mseuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo analowa nane kubwalo lakunja, ndipo taonani, panali zipinda, ndi moyalidwa miyala mokonzekera bwalo pozungulira ponse; moyalidwa miyalamo munali zipinda makumi atatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka munthuyo anandilowetsa mʼbwalo lakunja, ndipo ndinaona zipinda zina ndi msewu wa miyala wozungulira bwalo lonse. Zipinda zonse zinali makumi atatu ndipo zinkayangʼana msewuwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo analowa nane ku bwalo lakunja, ndipo taonani, panali zipinda, ndi moyalidwa miyala mokonzekera bwalo pozungulira ponse; moyalidwa miyalamo munali zipinda makumi atatu.