Ezekiel 40:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zipinda za alonda zimene zinali zitatu pa mbali iliyonse, mphuthu zake ndiponso khonde lake lam'kati, zonse zinali zolingana ndi za chipata choyamba chija. M'litali mwake chinali mamita 25, ndipo muufupi mwake chinali mamita 12 ndi theka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi zipinda zake ndizo zitatu chakuno, ndi zitatu chauko, ndi makhoma a pakati pake; ndi zidundumwa zake zinali monga mwa muyeso wa chipata choyambacho, m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zipinda za alonda zimene zinalipo zitatu mbali iliyonse, makoma ake ndi khonde zinali ndi muyeso wofanana ndi wachipata choyamba chija. Kutalika kwake kunali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi zipinda zace ndizo zitatu cakuno, ndi zitatu cauko, ndi makhoma a pakati pace; ndi zidundumwa zace zinali monga mwa muyeso wa cipata coyambaco, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.