Ezekiel 40:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mazenera ake, khonde lake lam'kati ndiponso kanjedza wozokota uja, zonse zinali zolingana ndi zachipata choyang'ana kuvuma. Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi aŵiri, ndipo khonde lake linali cham'kati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mazenera ake, ndi zidundumwa zake, ndi akanjedza ake, anali monga mwa muyeso wa chipata choloza kum'mawa; ndipo anakwerako ndi makwerero asanu ndi awiri, ndi zidundumwa zake zinali pakhomo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mipata yake, khonde lake ndi zojambula za kanjedza zinali ndi miyeso yofanana ndi za chipata chakummawa. Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndipo kotsirizira kwa chipatacho kunali khonde.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mazenera ace, ndi zidundumwa zace, ndi akanjedza ace, anali monga mwa muyeso wa cipata coloza kum'mawa; ndipo anakwerako ndi makwerero asanu ndi awiri, ndi zidundumwa zace zinali pakhomo.