Ezekiel 40:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chipata chonga chakuvuma chija chidakaloŵa ku bwalo lam'kati moyang'anana ndi chipata chakumpoto. Adachiyesa kuchokera ku chipata china mpaka ku chipata china, kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali chipata cha bwalo lam'kati, chopenyana ndi chipata chinzake chakunja kumpoto, ndi cha kum'mawa; ndipo anayesa kuyambira kuchipata kufikira kuchipata mikono zana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panalinso chipata cholowera ku bwalo lamʼkati chofanana ndi chakummawa chimene chimayangʼanana ndi chipata chakumpoto, chofanana ndi cha mbali ya kummawa. Anachiyeza kuchokera ku chipata china mpaka ku chipata china. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali cipata ca bwalo lam'kati, copenyana ndi cipata cinzace cakunja kumpoto, ndi ca kum'mawa; ndipo anayesa kuyambira kucipata kufikira kucipata mikono zana.