Ezekiel 40:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake munthu uja adapita nane kumwera, ndipo ndidaona chipata choyang'ana kumwera. Adayesa mphuthu zake ndi khonde lake lam'kati, zinali zolingana ndi zinzake zija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananditsogolera kunka kumwera, ndipo taonani, panali chipata kumwera, nayesa makhoma a pakati pake, ndi zidundumwa zake, monga mwa miyeso yomweyi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo munthuyo anapita nane ku mbali yakummwera ndipo ndinaona chipata chakummwera. Iye anayeza mphuthu zake ndi khonde ndipo zinali ndi miyeso yofanana ndi ya zina zija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananditsogolera kumka kumwela, ndipo taonani, panali cipata kumwela, nayesa makhoma a pakati pace, ndi zidundumwa zace, monga mwa miyeso yomweyi.