Ezekiel 40:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'zipinda za chipata chimenechi ndi m'khonde lake lam'kati munali mazenera onga a m'zipinda zina. M'litali mwake munali mamita 25, muufupi mwake munali mamita 12 ndi theka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zake pozungulirapo, monga mazenera ena aja, m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼzipinda za chipata cholowera chimenechi ndi mʼkhonde lake munali mipata yofanana ndi ya mʼzipinda zina. Mulitali mwake munali mamita 27, mulifupi mwake munali mamita 13.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zace pozungulirapo, monga mazenera ena aja, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.