Ezekiel 40:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panalinso makwerero asanu ndi aŵiri, ndipo khonde lake linali cham'kati. Pa mphuthu zake adaazokotapo zithunzi za kanjedza uku ndi uku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali makwerero asanu ndi awiri okwererapo, ndi zidundumwa zake kumaso kwake; ndi pa nsanamira zake chakuno ndi chauko panali akanjedza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndi khonde kotsirizira kwake. Chipindacho chinali ndi zojambula za kanjedza ku mbali zonse za makoma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali makwerero asanu ndi awiri okwererapo, ndi zidundumwa zace kumaso kwace; ndi pa nsanamira zace cakuno ndi cauko panali akanjedza.