Ezekiel 40:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu uja adandiloŵetsa m'bwalo lam'kati kudzera ku chipata chakumwera. Adayesa chipatacho, chinali cholingana ndi zinzake zija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo analowa nane pa chipata cha kumwera m'bwalo lam'kati, nayesa chipata cha kumwera, monga mwa miyeso yomweyi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo munthu uja anandilowetsa mʼbwalo lamʼkati kudzera ku chipata chakummwera. Anayeza chipatachi ndipo chinali chofanana ndi zinzake zija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo analowa nane pa cipata ca kumwela m'bwalo lam'kati, nayesa cipata ca kumwera, monga mwa miyeso yomweyi;