Ezekiel 40:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atandifikitsa kumeneko, ndidaona munthu wonyezimira ngati mkuŵa. M'manja mwake anali ndi chingwe chabafuta ndi bango loyesera, ndipo adaaimirira pa chipata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ake ngati amkuwa, ndi chingwe chathonje m'dzanja lake, ndi bango loyesa nalo, naima kuchipata iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atandifikitsa kumeneko ndinaona munthu wonyezimira ngati mkuwa. Iye anali atayima pa chipata ndipo mʼdzanja lake munali chingwe cha nsalu yabafuta ndi ndodo yoyezera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ace ngati amkuwa, ndi cingwe cabwazi m'dzanja lace, ndi bango loyesa nalo, naima kucipata iye.