Ezekiel 40:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zipinda zake, mphuthu zake ndiponso khonde lake lam'kati zinali zolingana ndi zinzake zija. Zipindazo zinali ndi mazenera kuzungulira ponse, ndiponso m'khonde mwake. M'litali mwake munali mamita 25, muufupi mwake mamita 12 ndi theka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi zipinda zake, ndi makhoma a pakati pake, ndi zikundumwa zake, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zake pozungulirapo, m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake chinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi zipindazace, ndi makhoma a pakati pace, Indi zikundumwa zace, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zace pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.