Ezekiel 40:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zipinda zake, mphuthu zake ndi khonde lake lam'kati zinali chimodzimodzi. Linali ndi mazenera kuzungulira ponse. M'litali mwake munali mamita 25, muufupi mwake mamita 12 ndi theka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
zipinda zake, makhoma a pakati pake, ndi zidundumwa zake; ndimo munali mazenera m'menemo pozungulirapo, m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zipinda zake za alonda, makoma ake ndiponso khonde lake zinali zofanana ndi zina zija, ndipo chinalinso ndi mipata mbali zonse ziwiri. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
zipinda zace, makhoma a pakati pace, ndi zidundumwa zace; ndimo munali mazenera m'menemo pozungulirapo, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.