Ezekiel 40:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthuyo adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, penyetsetsa ndipo umvetsetse bwinobwino. Uikepo mtima pa zonse zimene ndikukuwonetsa, pakuti chimenechi ndicho chifukwa chake chimene adakubweretsera kuno. Tsono ukaŵauze Aisraele zonse zimene uziwonezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m'makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israele zonse uziona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthuyo anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, penyetsetsa ndipo umvetse bwinobwino. Uyikepo mtima wako pa zonse zimene ndikukuonetsa pakuti anakubweretsa kuno kuti uwone zimenezi. Tsono ukawawuze Aisraeli zonse zimene uzione.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m'makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israyeli zonse uziona.