Ezekiel 40:44 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono munthu uja adapita nane m'kati mwenimweni mwa bwalo. Ndidaonamo zipinda ziŵiri m'kati mwa bwalolo. China chinali pafupi ndi chipata chakumpoto kuyang'ana kumwera. China chinali pafupi ndi chipata chakumwera kuyang'ana kumpoto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi kunja kwa chipata cha m'kati kunali tinyumba ta oimba m'bwalo lam'kati, kumbali ya chipata cha kumpoto; ndipo tinaloza kumwera, kena kumbali ya chipata cha kum'mawa kanaloza kumpoto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu uja anapita nane mʼkati mwa bwalo ndipo ndinaona zipinda ziwiri. Chimodzi chinali pafupi ndi chipata chakumpoto kuyangʼana kummwera ndi china chinali pafupi ndi chipata chakummwera kuyangʼana kumpoto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi kunja kwa cipata ca m'kati kunali tinyumba ta oyimba m'bwalo lam'kati, ku mbali ya cipata ca kumpoto; ndipo tinaloza kumwela, kena ku mbali ya cipata ca kum'mawa kanaloza kumpoto.