Ezekiel 40:46 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chipinda choyang'ana kumpotochi ncha ansembe oyang'anira za guwa lansembe. Ameneŵa ndiwo ana a Zadoki, ndipo ndi okhawo mwa zidzukulu za Levi amene angafike kufupi kudzatumikira Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi kanyumba koloza kumpoto nka ansembe odikira guwa la nsembe, ndiwo ana a Zadoki amene ayandikira kwa Yehova mwa ana a Levi, kumtumikira Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo chipinda chimene chikuyangʼana kumpoto ndi cha ansembe amene amayangʼanira guwa lansembe. Amenewa ndiwo ana a Zadoki, ndipo ndi okhawo mwa zidzukulu za Levi amene ayenera kutumikira pamaso pa Yehova mʼNyumba ya Mulungu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi kanyumba koloza kumpoto nka ansembe odikira guwa la nsembe, ndiwo ana a Zadoki amene ayandikira kwa Yehova mwa ana a Levi, kumtumikira Iye.