Ezekiel 40:47 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono munthu uja adayesa bwalolo, linali lolingana m'litali ndi muufupi mwake, mamita 50 mbali iliyonse. Ndipo guwa linali kumaso kwa Nyumba ya Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayesa bwalolo mikono zana m'litali mwake, ndi mikono zana kupingasa kwake, laphwamphwa; ndi guwa la nsembe linali kukhomo kwa nyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka munthuyo anayeza bwalo; linali lofanana mbali zonse kutalika kwake, mulitali mwake munali mamita 53, ndipo mulifupi mwake munali mamita 53. Ndipo guwa lansembe linali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayesa bwalolo mikono zana m'litali mwace, ndi mikono zana kupingasa kwace, lamphwamphwa; ndi guwa la nsembe linali kukhomo kwa nyumba.