Ezekiel 40:48 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adapita nane m'khonde lam'kati la Nyumba ya Mulunguyo. Adayesa mphuthu za khondelo zinali za mamita aŵiri ndi theka mbali zonse. Muufupi mwake mwa chipata munali mamita asanu ndi aŵiri. Zipupa za pambali pa chipata zinali za mita limodzi ndi theka mbali zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anadza nane kukhonde la Kachisi, nayesa mphuthu za khonde, mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; ndi kupingasa kwa chipata, mikono itatu chakuno, ndi mikono itatu chauko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthuyo anapita nane pa khonde la Nyumba ya Mulunguyo. Anayeza mphuthu za khondelo ndipo zinali mamita awiri ndi theka mbali zonse. Mulifupi mwa chipatacho munali mamita asanu ndi awiri ndipo mulifupi mwa makoma ake munali mamita awiri mbali zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anadza nane ku khonde la kacisi, nayesa mphuthu za khonde, mikono isanu cakuno, ndi mikono isanu cauko; ndi kupingasa kwa cipata, mikono itatu cakuno, ndi mikono itatu cauko.