Ezekiel 40:49 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khonde lam'kati m'litali mwake linali la mamita khumi, muufupi mwake mamita asanu ndi limodzi. Panali makwerero khumi, ndipo pambali pa mphuthu panali nsanamira ku mbali zonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'litali mwake mwa khonde mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono khumi ndi umodzi; ndipo panali makwerero khumi okwerera kumeneko; ndipo panali zoimiritsa pa nsanamirazo, imodzi chakuno, ndi imodzi chauko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulitali mwa khonde munali mamita khumi, mulifupi mwake munali mamita asanu ndi limodzi kuchokera kutsogolo mpaka kumbuyo. Panali makwerero khumi, ndipo mbali zonse kunali nsanamira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'litali mwace mwa khonde mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwace mikono khumi ndi umodzi; ndipo panali makwerero khumi okwerera kumeneko; ndipo panali zoimiritsa pa nsanamirazo, imodzi cakuno, ndi imodzi cauko.