Ezekiel 40:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidaona chipupa chozinga Nyumba ya Mulungu ponseponse. Munthu uja anali ndi bango lopimira m'manja mwake. Bangolo kutalika kwake linali mamita atatu. Adapima kuchindikira kwa chipupacho napeza kuti ndi bango lathunthu. Kutalika kwake cham'mwamba kunalinso bango lathunthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taonani, panali linga kunja kwake kwa nyumba ya Kachisi poizinga, ndi m'dzanja lake la munthuyo bango loyesa nalo la mikono isanu ndi umodzi, mkono uliwonse mkono kudza chikhato; ndipo anayesa chimangidwecho kuchindikira kwake bango limodzi, ndi msinkhu wake bango limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinaona khoma litazungulira mbali zonse za Nyumba ya Mulungu. Mʼdzanja la munthuyo munali bango lopimira limene kutalika kwake kunali kwa mamita atatu. Atayeza chipupacho anapeza kuti kuchindikira kwake kunali mamita atatu, ndiponso kutalika kwake kunalinso mamita atatu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taonani, panali linga kunja kwace kwa nyumba ya kacisi poizinga, ndi m'dzanja lace la munthuyo bango loyesa nalo la mikono isanu ndi umodzi, mkono uli wonse mkono kudza cikhato; ndipo anayesa cimangidweco kucindikira kwace bango limodzi, ndi msinkhu wace bango limodzi.