Ezekiel 40:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panalinso zipinda za alonda, ndipo chilichonse chinali bango lathunthu m'litali mwake, chimodzimodzinso mu ufupi mwake, bango lathunthu. Mipata ya pakati pa zipindazo inali ya mamita aŵiri ndi theka. Ndipo chiwundo cha pachipata pafupi ndi khonde lam'kati lapachipata, chinali bango lathunthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi chipinda cha alonda, chonse ncha bango limodzi m'litali mwake, ndi bango limodzi kupingasa kwake, ndi pakati pa zipinda za alonda mikono isanu, ndi chiundo cha chipata kumbali ya kukhonde la kuchipata m'katimo, bango limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kudutsa chiwundo choyambachi, panali zipinda za alonda zisanu ndi chimodzi, zitatu kudzanja lamanja, zitatu kudzanja lamanzere. Chilichonse chinali cha mamita atatu mulitali mwake, chimodzimodzinso mulifupi mwake. Mipata ya pakati pa zipindazo inali ya mamita awiri ndi theka. Ndipo chiwundo cha pa chipata pafupi ndi khonde lapachipata, chinali mamita atatu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi cipinda ca alonda, conse nca bango limodzi m'litali mwace, ndi bango limodzi kupingasa kwace, ndi pakati pa zipinda za alonda mikono isanu, ndi ciundo ca cipata ku mbali ya ku khonde la kucipata m'katimo, bango limodzi.