Ezekiel 41:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake munthu uja adapita nane m'chipinda chopatulika cha Nyumba ya Mulungu, nayesa mphuthu zake. Muufupi mwake munali mamita atatu mbali iliyonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza nane ku Kachisi, nayesa nsanamira zake, kupingasa kwake mikono isanu ndi umodzi chakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi chauko, ndiko kupingasa kwa chihema chija.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo munthuyo anapita nane mʼchipinda chopatulika cha Nyumba ya Mulungu ndipo anayeza khonde lake; mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu mbali iliyonse kutalika kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza nane ku Kacisi, nayesa nsanamira zace, kupingasa kwace mikono isanu ndi umodzi cakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi cauko, ndiko kupingasa kwa cihema cija.