Ezekiel 41:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zipinda zam'mbalizo zinali zotsekulira ku mbali za chiwundo. Chitseko chimodzi chinkayang'ana kumpoto, china chinkayang'ana kumwera. Kukula kwa chiwundo chosamangapo kanthu kunali mamita aŵiri ndi theka kuzungulira ponseponse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi makomo a zipinda za m'mphepete analoza kumpatawo, khomo lina kumpoto, ndi lina kumwera; ndi malo a pa mpatawo anayesa mikono isanu kupingasa kwake pozungulira pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitseko za zipinda zamʼmbalizo zinali zotsekulira ku chiwundo. Chitseko chimodzi chinkayangʼana kumpoto ndipo china chinkayangʼana kummwera. Chiwundo chosamangapo kanthu chinali mamita awiri ndi theka kukula kwake kuzungulira ponseponse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi makomo a zipinda za m'mphepete analoza kumpatawo, khomo lina kumpoto, ndi lina kumwela; ndi malo a pa mpatawo anayesa mikono isanu kupingasa kwace pozungulira pace.