Ezekiel 41:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chakuzambwe, kuyang'anana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu, kunali nyumba inanso ya mamita 35 muufupi mwake. Khoma lake linali la mamita aŵiri ndi theka kuchindikira kwake kuzungulira ponseponse, m'litali mwake linali la mamita 45.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nyumba inali kutsogolo kwa mpata wa mbali ya kumadzulo inali ya mikono makumi asanu ndi awiri kupingasa kwake; ndi khoma la nyumbayo pozungulira pake linali la mikono isanu kuchindikira kwake; ndi m'litali mwake mikono makumi asanu ndi anai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nyumba imene inali chakummwera moyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu inali mamita 35 mulifupi mwake. Khoma la nyumbayo linali mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake kuzungulira ponseponse, ndipo mulitali mwake linali mamita 45.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nyumba inali kutsogolo kwa mpata wa mbali ya kumadzulo inali ya mikono makumi asanu ndi awiri kupingasa kwace; ndi khoma la nyumbayo pozungulira pace linali la mikono isanu kucindikira kwace; ndi m'litali mwace mikono makumi asanu ndi anai.